Luke 23:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adaŵauza kuti, “Mwadzampereka munthuyu kwa ine kuti ndi munthu wosokeza anthu. Ndipo onani, ine ndamufunsa pamaso panu, koma sindikumpeza mlandu pa zonse zimene mukumnenezazi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
nati kwa iwo, Munadza kwa ine ndi munthu uyu ngati munthu wakupandutsa anthu: ndipo taonani, Ine ndinamfunsa za mlanduwu pamaso panu, ndipo sindinapeza pa munthuyu chifukwa cha zinthu zimene mumnenera;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
ndipo anawawuza kuti, “Munabweretsa munthuyu kwa ine ngati ndiye amawuza anthu kuti awukire. Ine ndamufunsa pamaso panu ndipo sindinapeze chomuyimbira mlandu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
nati kwa iwo, Munadza kwa ine ndi munthu uyu ngati munthu wakupandutsa anthu: ndipo taonani, Ine ndinamfunsa za mlanduwu pamaso panu, ndipo sindinapeza pa munthuyu cifukwa ca zinthu zimene mumnenera;