Luke 23:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iwo adayamba kuneneza Yesu kuti, “Munthu uyu tidampeza akusokeza anthu a mtundu wathu. Amatiletsa kuti tisamakhome msonkho kwa Mfumu ya ku Roma. Amanenanso kuti ati Iyeyu ndi Mpulumutsi wolonjezedwa uja ndiponso mfumu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anayamba kumnenera Iye, kuti, Tinapeza munthu uyu alikupandutsa anthu a mtundu wathu, ndi kuwaletsa kupereka msonkho kwa Kaisara, nadzinenera kuti Iye yekha ndiye Khristu mfumu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo iwo anayamba kumuneneza nati, “Ife tinapeza munthu uyu akusokoneza anthu a mtundu wathu ndipo amatsutsa zopereka msonkho kwa Kaisara komanso amati ndi Khristu, Mfumu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anayamba kumnenera iye, kuti, Tinapeza munthu uyu alikupandutsa anthu a mtundu wathu, ndi kuwaletsa kupereka msonkho kwa Kaisara, nadzinenera kuti iye yekha ndiye Kristu mfumu.