Luke 23:22 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pilato adaŵafunsa kachitatu kuti, “Koma wachimwanji Iyeyu? Sindikumpeza mlandu woyenera kumuphera. Motero ndingomukwapula kenaka ndimmasula.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anati kwa iwo nthawi yachitatu, Nanga munthuyu anachita choipa chiyani? Sindinapeza chifukwa cha kufera Iye; chotero ndidzamkwapula Iye ndi kummasula.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kachitatu anawafunsanso iwo kuti, “Chifukwa chiyani? Kodi munthu uyu wachita choyipa chanji? Ine sindinapeze cholakwa mwa Iye chakuti aphedwe choncho ndingomukwapula ndi kumumasula.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anati kwa iwo nthawi yacitatu, Nanga munthuyu anacita coipa ciani? Sindinapeza cifukwa ca kufera iye; cotero ndidzamkwapula iye ndi kummasula.