Luke 23:35 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu ena onse adaimirira pomwepo nkumaonerera. Komanso akulu a Ayuda ankamunyodola nkumanena kuti, “Adapulumutsa ena, adzipulumutse yekha ngati ndiyedi Mpulumutsi uja amene Mulungu adamsankha.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anthu anaima alikupenya. Ndi akulunso anamlalatira Iye, nanena, Anapulumutsa ena; adzipulumutse yekha ngati iye ndiye Khristu wa Mulungu, wosankhidwa wake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu anayimirira nʼkumaonerera, ngakhalenso akuluakulu ankamulalatira Iye. Iwo anati, “Iye anapulumutsa ena; adzipulumutse yekha ngati ndi Khristu wa Mulungu, Wosankhidwayo.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anthu anaima alikupenya, Ndi akurunso anamlalatira iye nanena, Anapulumutsa ena; adzipulumutse yekha ngati iye ndiye Kristu wa Mulungu, wosankhidwa wace.