Luke 23:48 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu onse amene adaasonkhana kudzaonerera zimene zinkachitikazo, ataona zonsezi, adabwerera kwao akudzigunda pa chifuwa ndi chisoni.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo makamu onse osonkhana kudzapenya ichi, pamene anaona zinachitikazo, anapita kwao ndi kudziguguda pachifuwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu onse amene anasonkhana kudzaonerera izi, ataona zinachitikazo, anadziguguda pachifuwa ndipo anachoka.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo makamu onse osonkhana kudzapenya ici, pamene anaona zinacitikazo, anapita kwao ndi kudziguguda pacifuwa.