Luke 23:55 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Azimai aja amene adaabwera ndi Yesu kuchokera ku Galileya, adatsatira Yosefe, naona manda ndi m'mene adaaikira mtembo wa Yesu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo akazi, amene anachokera naye ku Galileya, anatsata m'mbuyo, naona manda, ndi maikidwe a mtembo wake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Amayi amene anabwera ndi Yesu kuchokera ku Galileya, anatsata Yosefe ndipo anaona manda ndi momwe mtembo wake anawuyikira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo 5 akazi, amene anacokera naye ku Galileya, anatsata m'mbuyo, naona manda, ndi maikidwe a mtembo wace.