Luke 24:17 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Yesu adaŵafunsa kuti, “Kodi mukunka mukukambirana zotani panjira pano?” Apo iwo adaima, nkhope zao zili zakugwa ndi chisoni,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anati kwa iwo, Mau awa ndi otani mulandizanawo poyendayenda? Ndipo anaima ndi nkhope zao zachisoni.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anawafunsa kuti, “Kodi mukukambirana zotani mʼnjira muno?” Iwo anayima ndi nkhope zakugwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anati kwa iwo, Mau awa ndi otani mulandizanawo poyendayenda? Ndipo anaima ndi nkhope zao zacisoni.