Luke 24:39 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Onani manja anga ndi mapazi anga, kuti ndine ndithu. Khudzeni muwone, paja mzukwa ulibe mnofu ndi mafupa monga mukuwona kuti Ine ndili nazo.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Penyani manja anga ndi mapazi anga, kuti Ine ndine mwini: ndikhudzeni, ndipo penyani; pakuti mzimu ulibe mnofu ndi mafupa, monga muona ndili nazo Ine.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Taonani manja anga ndi mapazi anga. Ine ndine amene! Khudzeni kuti muone. Mzukwa ulibe mnofu ndi mafupa monga mukuonera ndili nazo.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Penyani manja anga ndi mapazianga, kuti Ine ndine mwini: 2 ndikhudzeni, ndipo penyani; pakuti mzimu ulibe, mnofu ndi mafupa, monga muona ndirinazo Ine.