Luke 24:44 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kenaka adaŵauza kuti, “Nzimenezitu zimene ndinkakuuzani pamene ndinali nanu. Paja ndinkanena kuti zonse ziyenera kuchitikadi zimene zidalembedwa za Ine m'Malamulo a Mose, m'mabuku a aneneri, ndi m'buku la Masalimo.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anati kwa iwo, Awa ndi mauwo ndinalankhula nanu, paja ndinakhala ndi inu, kuti ziyenera kukwanitsidwa zonse zolembedwa za Ine m'chilamulo cha Mose, ndi aneneri, ndi Masalmo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anawawuza kuti, “Izi ndi zimene ndinakuwuzani pamene ndinali nanu: chilichonse chiyenera kukwaniritsidwa chimene chinalembedwa cha Ine mʼbuku la Malamulo a Mose, Aneneri ndi Masalimo.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anati kwa iwo, 5 Awa ndi mauwo ndinalankhula nanu, paja ndinakhala ndi inu, kuti ziyenera kukwanitsidwa zonse zolembedwa za Ine m'cilamulo ca 6 Mose, ndi aneneri, ndi masalmo.