Luke 3:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pa chaka cha khumi ndi chisanu cha ufumu wa Tiberio, mfumu ya ku Roma, Ponsio Pilato anali bwanamkubwa ku Yudeya. Herode ankalamulira ku dera la Galileya. Filipo, mbale wake, ankalamulira ku dera la Itureya ndi ku dera la Trakoniti. Lisaniasi ankalamulira ku dera la Abilene,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pa chaka chakhumi ndi chisanu cha ufumu wa Tiberio Kaisara, pokhala Pontio Pilato kazembe wa Yudeya, ndi Herode chiwanga cha Galileya, ndi Filipo mbale wake chiwanga cha dziko la Itureya ndi la Trakoniti, ndi Lisaniasi chiwanga cha Abilene;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mʼchaka cha 15 mu ulamuliro wa Tiberiyo Kaisara, Pontiyo Pilato ali bwanamkubwa wa Yudeya, Herode ankalamulira ku Galileya, mʼbale wake Filipo ankalamulira ku Iturea ndi ku dera la Trakoniti, ndipo Lusaniyo ankalamulira ku Abilene.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pa caka cakhumi ndi cisanu ca ufumu wa Tiberiyo Kaisara, pokhala Pontiyo Pilato kazembe wa Yudeya, ndi Herode ciwanga ca Galileya, ndi Filipo mbale wace ciwanga ca dziko la Itureya ndi la Trakoniti, ndi Lusaniyo ciwanga ca Abilene;