Luke 3:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Asilikali omwe adamufunsa kuti, “Nanga ifeyo tizichita zabwino zanji?” Iye adati, “Musamalanda za munthu aliyense pakuwopseza kapena pakumnamizira. Muzikhutira ndi malipiro anu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo asilikali omwe anamfunsa iye, nati, Nanga ife tizichita chiyani? Ndipo iye anati kwa iwo, Musaopse, musanamize munthu aliyense; khalani okhuta ndi kulipira kwanu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka asilikali ena anamufunsa kuti, “Nanga ife tichite chiyani?” Iye anayankha kuti, “Musamalande ndalama moopseza ndipo musamanamizire anthu, khutitsidwani ndi malipiro anu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo asilikari omwe anamfunsa iye, nati, Nanga ife tizicita ciani? Ndipo iye anati kwa iwo, Musaopse, musanamize munthu ali yense; khalani okhuta ndi kulipira kwanu.