Luke 3:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Izi zidachitika monga zidaalembedwera m'buku la mneneri Yesaya kuti, “Liwu la munthu wofuula m'chipululu: akunena kuti, ‘Konzani mseu wodzadzeramo Ambuye, ongolani njira zoti adzapitemo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
monga mwalembedwa m'buku la Yesaya mneneri, kuti, Mau a wofuula m'chipululu, konzani khwalala la Ambuye, lungamitsani njira zake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Monga analembera mʼbuku la Yesaya mneneri kuti: “Mawu a wofuwula mʼchipululu, konzani njira ya Ambuye, wongolani njira zake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
monga mwalembedwa m'kalata wa mau a Yesaya mneneri, kuti, Mau a wopfuula m'cipululu, Konzani khwalala la Ambuye, Lungamitsani njira zace.