Luke 3:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu ambirimbiri ankabwera kuti iye aŵabatize. Tsono iyeyo ankati, “Ana a njoka inu, adakuchenjezani ndani kuti muthaŵe chilango cha Mulungu chikudzachi?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake iye ananena kwa makamuwo a anthu amene anatulukira kukabatizidwa ndi iye, Obadwa a njoka inu, anakulangizani inu ndani kuthawa mkwiyo ulinkudza?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yohane anati kwa magulu a anthu amene amabwera kudzabatizidwa ndi iye, “Ana anjoka inu! Anakuchenjezani ndani kuti muthawe mkwiyo umene ukubwera?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace iye ananena kwa makamuwo a anthu amene anaturukira kukabatizidwa ndi iye, Obadwa a njoka inu, anakulangizani inu ndani kuthawa mkwiyo ulinkudza?