Luke 3:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chitanitu ntchito zosonyeza kuti mwatembenukadi mtima. Ndipo m'mitima mwanu musayambe zomanena kuti, ‘Atate athu ndi Abrahamu.’ Ndithu ndikunenetsa kuti Mulungu angathe kusandutsa ngakhale miyala ili apayi kuti ikhale ana a Abrahamu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake balani zipatso zakuyenera kulapa mtima, ndipo musayambe kunena mwa inu nokha, Atate wathu tili naye ndiye Abrahamu: pakuti ndinena kwa inu, kuti ali ndi mphamvu Mulungu, mwa miyala iyi, kuukitsira Abrahamu ana.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Onetsani zipatso zakutembenuka mtima, ndipo musamanene mwa inu nokha kuti, ‘Tili nalo kholo lathu Abrahamu,’ pakuti ndikuwuzani kuti kuchokera ku miyala iyi, Mulungu akhoza kumuwutsira Abrahamuyo ana.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace balani zipatso zakuyenera kulapa mtima, ndipo musayambe kunena mwa inu nokha, Atate wathu tiri naye ndiye Abrahamu: pakuti ndinena kwa inu, kuti ali ndi mphamvu Mulungu, mwa miyala iyi, kuukitsira Abrahamu ana.