Luke 4:18 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Mzimu wa Chauta wadzaza mwa Ine. Wandidzoza kuti ndikalalikire amphaŵi Uthenga Wabwino. Wandituma kuti ndikalengeze kwa am'ndende kuti adzamasulidwa, ndi kwa akhungu kuti adzapenyanso. Wandituma kuti ndikaŵapatse ufulu anthu osautsidwa,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mzimu wa Ambuye uli pa Ine, chifukwa chake Iye anandidzoza Ine ndiuze anthu osauka Uthenga Wabwino: anandituma Ine kulalikira am'nsinga mamasulidwe, ndi akhungu kuti apenyanso, kutulutsa ndi ufulu ophwanyika,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Mzimu wa Ambuye ali pa Ine; chifukwa wandidzoza kuti ndilalikire Uthenga Wabwino kwa osauka. Wandituma kuti ndilalikire kwa a mʼndende kuti amasulidwe ndi kwa osaona kuti apenyenso, kumasulidwa kwa osautsidwa,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mzimu wa Ambuye uli paine, Cifukwa cace iye anandidzoza Ine ndiuze anthu osauka Uthenga Wabwino: Anandituma Ine kulalikira am'nsinga mamasulidwe, Ndi akhungu kuti apenyenso, Kuturutsa ndi ufuru ophwanyika,