Luke 4:25 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kunena zoona, paja panali azimai amasiye ambiri pakati pa Aisraele pa nthaŵi ya mneneri Eliya, pamene mvula siidagwe zaka zitatu ndi miyezi isanu ndi umodzi, kotero kuti munali njala yaikulu m'dziko lonse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma zoonadi ndinena kwa inu, kuti, Munali akazi amasiye ambiri m'Israele masiku ake a Eliya, pamene kunatsekedwa kumwamba zaka zitatu ndi miyezi isanu ndi umodzi, pamene panakhala njala yaikulu pa dziko lonselo;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ine ndikukutsimikizirani kunali amayi ambiri amasiye mu Israeli mʼnthawi ya Eliya, kumwamba kutatsekedwa kwa zaka zitatu ndi theka ndipo kunali njala yayikulu mʼdziko lonselo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma zoonadi ndinena kwa inu, kuti, Munali akazi amasiye ambiri m'lsrayeli masiku ace a Eliya, pamene kunatsekedwa kumwamba zaka zitatu ndi miyezi isanu ndi umodzi, pamene panakhala njala yaikuru pa dziko lonselo;