Luke 4:27 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Panalinso akhate ambiri pakati pa Aisraele nthaŵi ya mneneri Elisa, komabe panalibe ndi mmodzi yemwe mwa iwo aja amene adachiritsidwa. Amene adachiritsidwa ndi Namani yekha wa ku dziko la Siriya.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo munali akhate ambiri m'Israele masiku a Elisa mneneri; ndipo palibe mmodzi wa iwo anakonzedwa, koma Naamani yekha wa ku Siriya.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo kunali akhate ambiri ku Israeli mʼnthawi ya mneneri Elisa, koma panalibe mmodzi mwa iwo anachiritsidwa kupatula Naamani wa ku Siriya.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo munali akhate ambiri m'Israyeli masiku a Elisa mneneri; ndipo palibe mmodzi wa iwo anakonzedwa, koma Namani yekha wa ku Suriya.