Luke 4:29 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adaimirira namtulutsira kunja kwa mudzi, nkupita naye pamwamba pa phiri pamene adaamangapo mudzi wao. Adaati akamponye kunsi,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
nanyamuka namtulutsira Iye kunja kwa mudziwo, nanka naye pamutu pa phiri pamene panamangidwa mudzi wao, kuti akamponye Iye pansi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anayimirira namutulutsira kunja kwa mzindawo, ndipo anamutengera pamwamba pa phiri pamene mzindawo unamangidwapo, ndi cholinga chakuti amuponyere ku phompho.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
nanyamuka na mturutsira Iye kunja kwa mudziwo, nanka naye pamutu pa phiri pamene panamangidwa mudzi wao, kuti akamponye iye pansi.