Luke 4:36 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu onse aja adazizwa, mpaka kumafunsana kuti, “Mau ameneŵa ngotani? Ngakhale mizimu yoipitsa anthu yomwe akuilamula ndi mphamvu ndi ulamuliro, ndipo ikutulukadi.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anthu onse anadabwa, nalankhulana wina ndi mnzake, nanena, Mau amenewa ali otani? Chifukwa ndi ulamuliro ndi mphamvu angolamulira mizimu yonyansa, ndipo ingotuluka.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu onse anadabwa ndipo anati kwa wina ndi mnzake, “Kodi chiphunzitso ichi ndi chotani? Ndi ulamuliro ndi mphamvu Iye akulamulira mizimu yoyipa ndipo ikutuluka!”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anthu onse anadabwa, nalankhulana wina ndi mnzace, nanena, Mau amenewa ali otani? cifukwa ndi ulamuliro ndi mphamvu angolamulira mizimu yonyansa, ndipo ingoturuka.