Luke 4:40 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Dzuŵa likuloŵa, anthu onse amene anali ndi anzao odwala nthenda zosiyanasiyana, adabwera nawo kwa Yesu. Iye adasanjika manja pa wodwala aliyense, naŵachiritsa onse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pakulowa dzuwa anthu onse amene anali nao odwala ndi nthenda za mitundumitundu, anadza nao kwa Iye; ndipo Iye anaika manja ake pa munthu aliyense wa iwo, nawachiritsa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamene dzuwa linkalowa, anthu anabweretsa kwa Yesu onse amene anali ndi matenda osiyanasiyana, ndipo atasanjika manja ake pa aliyense, anachiritsidwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pakulowa dzuwa anthu onse amene anali nao odwala ndi nthenda za mitundu mitundu, anadza nao kwa iye; ndipo iye anaika manja ace pa munthu ali yense wa iwo, nawaciritsa.