Luke 4:41 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nayonso mizimu yoipa inkatuluka mwa anthu ambiri ikufuula nkumanena kuti, “Inu ndinu Mwana wa Mulungu.” Koma Iye adaidzudzula, osailola kuti ilankhule, chifukwa idaadziŵa kuti analidi Mpulumutsi wolonjezedwa uja.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi ziwanda zomwe zinatuluka mwa ambiri, ndi kufuula, kuti, Inu ndinu Mwana wa Mulungu. Ndipo Iye anazidzudzula, wosazilola kulankhula, chifukwa zinamdziwa kuti Iye ndiye Khristu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Komanso ziwanda zinkatuluka mwa anthu ambiri, zikufuwula kuti, “Inu ndinu Mwana wa Mulungu!” Koma Iye anazidzudzula ndipo sanazilole kuyankhula chifukwa zimadziwa kuti Iye ndi Khristu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi ziwanda zomwe zinaturuka mwa ambiri, ndi kupfuula, kuti, Inu ndinu Mwana wa Mulungu. Ndipo iye anazidzudzula, wosazilola kulankhula, cifukwa zinamdziwa kuti iye ndiye Kristu.

Recommended Reading