Luke 4:42 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kutacha, Yesu adachoka ku Kapernao kuja napita ku malo kosapitapita anthu. Makamu a anthu adayamba kumufunafuna, ndipo atampeza, adayesa kumletsa kuti asaŵasiye.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kutacha anatuluka Iye nanka kumalo achipululu; ndi makamu a anthu analikumfunafuna Iye, nadza nafika kwa Iye, nayesa kumletsa Iye, kuti asawachokere.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kutacha, Yesu anapita ku malo a yekha. Anthu ankamufunafuna Iye ndipo pamene anafika kumene anali, anthuwo anayesetsa kumuletsa kuti asawachokere.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kutaca anaturuka iye nanka ku malo acipululu; ndi makamu a anthu analikwnfunafuna iye, nadza nafika kwa iye, nayesa kumletsa iye, kuti asawacokere.