Luke 5:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Yesu adamuuza kuti, “Chenjera, usakambire wina aliyense zimenezi. Ingopita, ukadziwonetse kwa wansembe ndipo ukapereke nsembe adalamula Mose ija. Imeneyo ikhale yotsimikizira anthu onse kuti wachiradi.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Iye anamuuzitsa, kuti asanene kwa munthu aliyense; koma uchoke, nudzionetse wekha kwa wansembe, nupereke nsembe ya pa chikonzedwe chako, monga adalamulira Mose, kukhale umboni kwa iwo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka Yesu anamulamula kuti, “Usawuze wina aliyense, koma pita, kadzionetse kwa wansembe ndi kukapereka nsembe zimene Mose anakulamulirani za kuyeretsedwa kwanu monga umboni kwa iwo.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo iye anamuuzitsa, kuti asanene kwa munthu ali yense; koma ucoke, nudzionetse wekha kwa wansembe, nupereke nsembe ya pa cikonzedwe cako, monga adalamulira Mose, kukhale umboni kwa iwo.