Luke 5:18 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono kudafika anthu ena ndi munthu wofa ziwalo, atamnyamulira pa machira. Adayesa kuloŵa naye m'nyumba kuti amkhazike pamaso pa Yesu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo onani, anthu alikunyamulira pakama munthu wamanjenje; nafunafuna kulowa naye, ndi kumuika pamaso pa Iye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Amuna ena anabwera atanyamula munthu wofa ziwalo pa mphasa ndipo anayesa kumulowetsa mʼnyumba kuti amugoneke pamaso pa Yesu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo onani, anthu alikunyamulira pakama munthu wamanjenje; nafunafuna kulowa naye, ndi kumuika pamaso pa iye.