Luke 5:21 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo aphunzitsi a Malamulo ndi Afarisi aja adayamba kudzifunsa mumtima mwao kuti, “Ndaninso kodi amene akunyoza Mulungu mwachipongweyu? Ndani angakhululukire machimo, si Mulungu yekha kodi?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo alembi ndi Afarisi anayamba kuyesayesa mumtima mwao, kuti, Ndani Uyu alankhula zomchitira Mulungu mwano? Ndani angathe kukhululukira machimo, koma Mulungu yekha?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Afarisi ndi aphunzitsi amalamulo anayamba kuganiza mwa iwo okha kuti, “Kodi munthu uyu ndi ndani amene ayankhula zamwano? Kodi ndani amene angakhululukire machimo kupatula Mulungu?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo alembi ndi Afarisi anayamba kuyesayesa mumtima mwao, kuti, ndani Uyu alankhula zomcitira Mulungu mwano? Ndani angathe kukhululukira macimo, koma Mulungu yekha?