Luke 5:24 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma kuti mudziŵe kuti Mwana wa Munthu ali nazo mphamvu pansi pano zokhululukira machimo, onani.” Pamenepo adauza wofa ziwalo uja kuti, “Iwe, ndikuti dzuka, tenga machira ako, uzipita kumudzi.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma kuti mudziwe kuti Mwana wa Munthu ali nayo mphamvu pa dziko lapansi yakukhululukira machimo, (anati Iye kwa wamanjenjeyo), Ndinena kwa iwe, Tauka, nusenze kama wako, numuke kunyumba kwako.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma kuti inu mudziwe kuti Mwana wa Munthu ali ndi ulamuliro pa dziko lapansi wokhululukira machimo, Iye anati kwa munthu wofa ziwaloyo, “Ine ndikuwuza iwe kuti, ‘Imirira, nyamula mphasa ndipo uzipita kwanu.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma kuti mudziwe kuti Mwana wa munthu ali nayo mphamvu pa dziko lapansi yakukhululukira macimo, (anati iye kwa wamanjenjeyo), Ndinena kwa iwe, Tauka, nusenze kama wako, numuke kunyumba kwako.