Luke 5:26 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu onse aja adazizwa kwambiri, nayamba kutamanda Mulungu. Adagwidwa ndi mantha nati, “Taona zodabwitsa lero.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo chizizwo chinagwira anthu onse ndipo analemekeza Mulungu; nadzazidwa ndi mantha, nanena kuti, Lero taona zodabwitsa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Aliyense anadabwa ndi kuchita mantha ndipo anayamika Mulungu. Iwo anadabwa kwambiri ndipo anati, “Lero taona zinthu zosayiwalika.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo cizizwo cinagwira anthu onse, ndipo analemekeza Mulungu nadzazidwa ndi mantha, nanena kuti, Lero taona zodabwitsa.