Luke 5:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yesu adaloŵa m'chombo chimodzi, chimene chinali cha Simoni, nampempha kuti asunthire pang'ono ku nyanja. Adakhala pansi, ndipo ali m'chombo momwemo, adayamba kuŵaphunzitsa anthuwo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Iye analowa m'ngalawa imodzi, ndiyo yake ya Simoni, nampempha iye akankhe pang'ono. Ndipo anakhala pansi m'menemo, naphunzitsa m'ngalawa makamuwo a anthu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye analowa mʼbwato limodzi limene linali la Simoni, ndi kumupempha kuti alikankhire mʼkati mwa nyanja pangʼono. Kenaka Iye anakhala pansi nayamba kuphunzitsa anthu ali mʼbwatomo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo iye analowa m'ngalawa imodzi, ndiyo yace ya Simoni, nampempha iye akankhe pang'ono. Ndipo anakhala pansi m'menemo, naphunzitsa m'ngalawa makamuwo a anthu.