Luke 5:36 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yesu adaŵapheranso fanizo, adati, “Munthu sang'amba chigamba ku chovala chatsopano nkuchisokerera pa chovala chakale. Chifukwa akatero, waononga chovala chatsopanocho, ndipo chigamba chatsopanocho sichidzayenerana ndi chovala chakale chija.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Iye ananenanso fanizo kwa iwo, kuti, Palibe munthu ang'amba chigamba cha malaya atsopano, nachiphatika pa malaya akale; chifukwa ngati atero, angong'ambitsa atsopanowo, ndi chigamba cha atsopanowo sichidzayenerana ndi akalewo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anawawuza fanizo ili: “Palibe amene amangʼamba chigamba kuchokera pa chovala chatsopano ndi kuchisokerera pa chakale. Ngati atatero, ndiye kuti adzangʼamba chovala chatsopanocho, ndipo chigamba chochokera pa chovala chatsopano chija sichidzagwirizana ndi chakale.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo iye ananenanso fanizo kwa iwo, kuti, Palibe munthu ang'amba cigamba ca maraya arsopano, naciphatika pa maraya akale; cifukwa ngati atero, angong'ambitsa atsopanowo, ndi cigamba ca atsopanowo sicidzayenerana ndi akalewo.