Luke 5:37 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Ndiponso munthu sathira vinyo watsopano m'matumba achikopa akale. Chifukwa akatero, vinyo watsopanoyo amaphulitsa matumba aja. Choncho vinyoyo adzatayika, matumbawo nkutha ntchito.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo palibe munthu atsanulira vinyo watsopano m'matumba akale; chifukwa ngati atero, vinyo watsopanoyo adzaphulitsa matumba, ndipo ameneyo adzatayika, ndi matumba adzaonongeka.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo palibe amene amakhuthulira vinyo watsopano mʼmatumba a vinyo akale. Ngati atatero, vinyo watsopanoyo adzaphulitsa zikopazo, vinyo adzatayika ndipo zikopa za vinyozo zidzawonongeka.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo palibe munthu atsanulira vinyo watsopano m'matumba akale; cifukwa ngati atero, vinyo watsopanoyo adzaphulitsa matumba, ndipo ameneyo adzatayika, ndi matumba adzaonongeka.