Luke 5:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Atatsiriza kulankhula, adauza Simoni kuti, “Sunthirani kozamako, muponye makoka anu kuti muphe nsomba.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pamene Iye analeka kulankhula, anati kwa Simoni, Kankhira kwa kuya, nimuponye makoka anu kukasodza.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Atatha kuyankhula anati kwa Simoni, “Kankhirani kwa kuya ndipo muponye makhoka kuti mugwire nsomba.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pamene iye analeka kulankhula, anati kwa Simoni, Kankhira kwa kuya, nimuponye makoka anu kukasodza.