Luke 6:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adaŵayang'ana onsewo, kenaka adalamula munthu uja kuti, “Tambalitsa dzanja lako.” Iye adalitambalitsa, ndipo dzanja lakelo lidakhalanso bwino.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pamene anaunguzaunguza pa iwo onse, anati kwa iye, Tansa dzanja lako. Ndipo iye anatero, ndi dzanja lake linabwerera momwe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye atawayangʼana onsewo, anati kwa munthuyo, “Wongola dzanja lako.” Iye anaterodi, ndipo dzanja lake linachiritsidwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pamene anaunguza-unguza pa iwo onse, anati kwa iye, Tansa dzanja lako, Ndipo iye anatero, ndi dzanja lace lina; bwerera momwe.