Luke 6:17 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yesu adatsika phiri pamodzi ndi ophunzira ake, naima pa chidikha. Panali khamu lalikulu la ophunzira ake, ndi anthu ena ambirimbiri ochokera ku dera lonse la Yudeya ndi ku Yerusalemu, ndi ku mbali yakunyanja, ku Tiro, ndi ku Sidoni.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Iye anatsika nao, naima pachidikha, ndi khamu lalikulu la ophunzira ake, ndi unyinji waukulu wa anthu a ku Yudeya lonse ndi Yerusalemu, ndi a ku mbali ya nyanja ya ku Tiro ndi Sidoni, amene anadza kudzamva Iye ndi kudzachiritsidwa nthenda zao;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anatsika pamodzi ndi atumwiwo ndipo anayima pamalo athyathyathya. Gulu lalikulu la ophunzira ake, gulu lalikulu la anthu ochokera ku Yudeya konse, ku Yerusalemu ndi ochokera mʼmphepete mwa nyanja ya Turo ndi Sidoni anali pomwepo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo iye anatsika nao, naima pacidikha, ndi khamu lalikuru la ophunzira ace, nw unyinji waukuru wa anthu a ku Yudeya lonse ndi Yerusalemu, ndi a ku mbali ya nyanja ya ku Turo ndi Sidoni, amene anadza kudzamva iye ndi kudzaciritsidwa nthenda zao;