Luke 6:25 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndinu atsoka, amene mukukhuta tsopanonu, chifukwa mudzamva njala. Ndinu atsoka, amene mukukondwa tsopanonu, chifukwa mudzamva chisoni ndiponso mudzalira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tsoka inu okhuta tsopano! Chifukwa mudzamva njala. Tsoka inu, akuseka tsopano! Chifukwa mudzachita maliro ndi kulira misozi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsoka inu amene mukudya bwino tsopano, chifukwa mudzakhala ndi njala. Ndinu atsoka, amene mukusekerera tsopano, chifukwa mudzabuma ndi kulira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tsoka inu okhuta tsopano! cifukwa mudzamva njala, Tsoka inu, akuseka tsopano! cifukwa mudzacita maliro ndi kulira misozi.