Luke 6:34 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo ngati mukongoza okhawo amene mukudziŵa kuti adzakubwezerani, mungayembekeze kulandira mphotho yanji? Pajatu ngakhale anthu ochimwa amakongoza anzao ochimwa, kuti akalandirenso momwemo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ngati mukongoletsa kanthu kwa iwo amene muyembekeza kulandiranso, mudzalandira chiyamiko chotani? Pakuti inde anthu ochimwa amakongoletsa kwa ochimwa anzao, kuti alandirenso momwemo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo ngati mukongoza amene mukuyembekeza kuti abweza, mwapindula chiyani? Ngakhale ‘ochimwa’ amabwereketsa kwa ochimwa anzawo, ndipo amayembekezera kubwezeredwa zonse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo 2 ngati mukongoletsa kanthu kwa iwo amene muyembekeza kulandiranso, mudzalandira ciyamiko cotani? pakuti inde anthu ocimwa amakongoletsa kwa ocimwa anzao, kuti alandirenso momwemo.