Luke 6:42 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ungamuuze bwanji mbale wako kuti, ‘Mbale wanga, taima ntakuchotsa kachitsotso kali m'maso mwakoka,’ pamene iweyo sukuchiwona chimtengo chimene chili m'maso mwako momwe? Iwe wachiphamaso, yamba wachotsa chimtengo m'maso mwako, pamenepo ndiye udzatha kupenya bwino nkukachotsa kachitsotso kamene kali m'maso mwa mbale wako.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kapena ungathe bwanji kunena kwa mbale wako, Mbale iwe, leka ndichotse kachitsotso kali m'diso lako, wosayang'anira iwe mwini mtanda uli m'diso lako? Wonyenga iwe! Thanga wachotsa mtandawo m'diso lako, ndipo pomwepo udzayang'anitsa bwino kuchotsa kachitsotso ka m'diso la mbale wako.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kodi munganene bwanji kwa mʼbale wanu kuti, ‘Mʼbale nʼtakuchotsa kachitsotso mʼdiso mwako,’ pamene inu eni ake mukulephera kuona mtengo uli mʼdiso mwanu? Inu achiphamaso, yambani mwachotsa mtengo uli mʼdiso mwanu, ndipo kenaka mudzaona bwinobwino ndi kuchotsa kachitsotso mʼdiso la mʼbale wanu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
10 Kapena ungathe bwanji kunena kwa mbale wako, Mbale iwe, leka ndicotse kacitsotso kali m'diso lako, wosayang'anira iwe mwini mtanda uli m'diso lako? Wonyenga iwe! thanga wacotsa mtandawo m'diso lako, ndipo pomwepo udzayang'anitsa bwino kucotsa kacitsotso ka m'diso la mbale wako.