Luke 6:45 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Munthu wabwino amatulutsa zabwino m'chuma chabwino cha mumtima mwake. Nayenso munthu woipa amatulutsa zoipa m'chuma choipa cha mumtima mwake. Pajatu pakamwa pamalankhula zimene zadzaza mu mtima.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Munthu wabwino atulutsa zabwino m'chuma chokoma cha mtima wake; ndi munthu woipa atulutsa zoipa m'choipa chake: pakuti m'kamwa mwake mungolankhula mwa kuchuluka kwa mtima wake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Munthu wabwino amatulutsa zinthu zabwino zosungidwa mu mtima mwake, koma munthu oyipa amatulutsa zinthu zoyipa zosungidwa mu mtima mwake. Pakamwa pake pamayankhula zimene zadzaza mu mtima mwake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
13 Munthu wabwino aturutsa zabwino m'cuma cokoma ca mtima wace; ndi munthu woipa aturutsa zoipa m'coipa cace: pakuti m'kamwa mwace mungolankhula mwa kucuruka kwa mtima wace.