Luke 6:48 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Amafanafana ndi munthu womanga nyumba, amene adaakumba mozama, naika maziko pa thanthwe. Tsono chigumula chitafika, madzi ake adagunda nyumbayo, koma sadaigwedeze, chifukwa adaaimanga bwino.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Iye afanafana ndi munthu wakumanga nyumba, amene anakumba pansi ndithu, namanga maziko a nyumbayo pathanthwe; ndipo pamene panadza chigumula, mtsinje unagunda pa nyumbayo, ndipo sunakhoza kuigwedeza; chifukwa idamangika bwino.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye ali ngati munthu womanga nyumba, amene anakumba mozama nayika maziko ake pa mwala. Madzi osefukira atabwera ndi mphamvu, nawomba nyumbayo koma sinagwedezeka, chifukwa anayimanga bwino.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Iye afanafana ndi munthu wakumanga nyumba, amene anakumba pansi ndithu, namanga maziko a nyumbayo pathanthwe; ndipo pamene panadza cigumula, mtsinje unagunda pa nyumbayo, ndipo sunakhoza kuigwedeza; cifukwa idamangika bwino.