Luke 6:49 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma munthu wongomva mau anga, osaŵagwiritsa ntchito, amafanafana ndi munthu amene adaamanga nyumba pamwamba pa nthaka, osakumba maziko. Pamene madzi a chigumula adagunda nyumbayo, pompo idagwa, ndipo kuwonongeka kwake kunali kotheratu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma iye amene akumva, ndi kusachita, afanafana ndi munthu wakumanga nyumba pa nthaka yopanda maziko; pa imeneyo unagunda mtsinje, ndipo inagwa pomwepo; ndipo kugumuka kwake kwa nyumbayo kunali kwakukulu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma amene amamva mawu anga koma osawachita, akufanana ndi munthu amene anamanga nyumba yake koma yopanda maziko. Nthawi yomwe madziwo anawomba nyumbayo, inagwa ndipo inawonongekeratu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma iye amene akumva, ndi kusacita, afanafana ndi munthu wakumanga nyumba pa nthaka yopanda maziko; pa imeneyo unagunda mtsinje, ndipo inagwa pomwepo; ndipo kugumuka kwace kwa nyumbayo kunali kwakukuru.