Luke 6:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Aphunzitsi a Malamulo ndi Afarisi ankafuna chifukwa choti akamnenezere Yesuyo, motero ankamuyang'anitsitsa kuti aone ngati achiritse munthu pa tsiku la Sabata.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo alembi ndi Afarisi analikumzonda Iye, ngati adzachiritsa tsiku la Sabata; kuti akapeze chomneneza Iye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Afarisi ndi aphunzitsi amalamulo ankamuyangʼana kuti apeze chifukwa Yesu, choncho anamuyangʼanitsitsa kuti aone ngati Iye akanamuchiritsa pa Sabata.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo alembi ndi Afarisi analikumzonda iye, ngati adzaciritsa tsiku la Sabata; kuti akapeze comneneza iye.