Luke 6:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Yesu adaadziŵa maganizo ao, tsono adalamula munthu wopuwala dzanja uja kuti, “Tabwera, udzaime kutsogolo kuno.” Iye adanyamuka nakaima kutsogoloko.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma Iye anadziwa maganizo ao; nati kwa munthuyo wa dzanja lake lopuwala, Nyamuka, nuimirire pakatipo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Yesu anadziwa zimene ankaganiza ndipo anati kwa munthu wadzanja lolumalayo, “Tanyamuka ndipo uyime patsogolo pa onsewa.” Choncho iye ananyamuka nayima pamenepo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma iye anadziwa maganizo ao; nati kwa munthuyo wa dzanja lace lopuwala, Nyamuka, nuimirire pakatipo.