Luke 7:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamene Yesu ankayandikira chipata cha mudziwo, adakumana ndi anthu atanyamula maliro. Womwalirayo anali mwana wamwamuna. Mai wake wa mwanayo anali wamasiye, ndipo mwana wake anali yekhayo. Anthu ambirimbiri am'mudzimo anali naye.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pamene anayandikira kuchipata cha mudziwo, onani, anthu analikunyamula munthu wakufa, mwana wamwamuna mmodzi yekha, amake ndiye mkazi wamasiye; ndipo anthu ambiri akumudzi anali pamodzi naye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Akufika pa chipata cha mudziwo, anakumana ndi anthu amene ankatuluka ndi munthu wakufa amene anali mwana yekhayo wa mkazi wamasiye. Gulu lalikulu la anthu a mʼmudziwo linali naye.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pamene anayandikira ku cipata ca mudziwo, onani, anthu analikunyamula munthu wakufa, mwana wamwamuna mmodzi yekha, amace ndiye mkazi wamasiye; ndipo anthu ambiri a kumudzi anali pamodzi naye.