Luke 7:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu onse adachita mantha, nayamba kutamanda Mulungu. Adati, “Mneneri wamkulu waoneka pakati pathu.” Adatinso, “Mulungu wadzathandiza anthu ake.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mantha anagwira onsewo: ndipo analemekeza Mulungu, nanena kuti, Mneneri wamkulu wauka mwa ife; ndipo Mulungu wadzacheza ndi anthu ake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Onse anachita mantha kwambiri nalemekeza Mulungu. Iwo anati, “Mneneri wamkulu waonekera pakati pathu. Mulungu wabwera kudzathandiza anthu ake.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mantha anagwira onsewo: ndipo analemekeza Mulungu, nanena kuti, Mneneri wamkuru wauka mwa ife; ndipo Mulungu wadzaceza ndi anthu ace.