Luke 7:20 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamene iwo adafika kwa Yesu, adamuuza kuti, “Yohane Mbatizi watituma kwa Inu kuti tidzakufunseni kuti, ‘Kodi Inuyo ndinu uja ankati adzabwerayu, kapena tiziyembekezera wina?’ ”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pakufika kwa Iye anthu awo, anati, Yohane Mbatizi watituma ife kwa Inu, kuti, Kodi ndinu wakudzayo, kapena tiyang'anire wina?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthuwo atafika kwa Yesu anati, “Yohane Mʼbatizi watituma kwa Inu kuti tidzafunse kuti, ‘Kodi ndinu anayenera kubwerayo, kapena tiyembekezere wina?’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pakufika kwa iye anthu awo, anati, Yohane Mbatizi watituma ife kwa Inu, kuti, Kodi ndinu wakudzayo, kapena tiyang'anire wina?