Luke 7:21 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nthaŵi imeneyo nkuti Yesu akuchiritsa kumene nthenda zosiyanasiyana za anthu ambiri. Ankatulutsa mizimu yoipa, nkumapenyetsa anthu akhungu ambiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nthawi yomweyo Iye anachiritsa anthu ambiri nthenda zao, ndi zovuta, ndi ziwanda; napenyetsanso anthu akhungu ambiri.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pa nthawi yomweyo, Yesu anachiritsa ambiri amene ankavutika, odwala ndi amene anali mizimu yoyipa, ndiponso anapenyetsa anthu osaona.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nthawi yomweyo iye anaciritsa anthu ambiri nthenda zao, ndi zobvuta, ndi mizimu yoipa; napenyetsanso anthu akhungu ambiri.