Luke 7:28 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Ndithu ndikunenetsa kuti mwa anthu onse amene adabadwa pansi pano, palibe ndi mmodzi yemwe woposa Yohane. Komabe ngakhale amene ali wamng'onong'ono mu Ufumu wa Mulungu amampambana.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndinena kwa inu, kuti, Mwa akubadwa ndi akazi palibe mmodzi wamkulu woposa Yohane; koma iye amene ali wamng'ono mu Ufumu wa Mulungu amposa iye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ine ndikukuwuzani kuti pakati pa obadwa kuchokera mwa mkazi palibe wina wamkulu kuposa Yohane; komabe amene ali wamngʼono mu ufumu wa Mulungu ndi wamkulu kuposa iye.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndinena kwa inu, kuti, Mwa akubadwa ndi akazi palibe mmodzi wamkuru woposa Yohane; koma iye amene ali wamng'ono mu Ufumu wa Mulungu amposa iye.