Luke 7:32 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ali ngati ana okangana pa msika, ena akufunsa anzao kuti, “ ‘Tidaakuimbirani ng'oma yaukwati, bwanji inu osavina? Tidaabuma maliro, bwanji inu osalira?’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Angofanana ndi ana akukhala pamsika, ndi kuitanizana wina ndi mnzake, ndi kunena, Ife tinakulizirani chitoliro, ndipo inu simunavina ai; tinabuma maliro, ndimo simunalira ai.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ali ngati ana amene akukangana pa msika, ena akufunsa anzawo kuti, “ ‘Ife tinakuyimbirani chitoliro, koma inu simunavine. Tinakuyimbirani nyimbo zamaliro, koma inu simunalire.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Angofanana ndi ana akukhala pamsika, ndi kuitanizana wina ndi mnzace, ndi kunena, Ife tinakulizirani citoliro, ndipo inu simunabvina ai; tinabuma maliro, ndimo simunalira ai.