Luke 7:36 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Wina wa m'gulu la Afarisi adaitana Yesu kuti akadye kwao. Yesu adapita nakaloŵa m'nyumba ya Mfarisiyo nkukakhala podyera.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mmodzi wa Afarisi anamuitana Iye kuti akadye naye. Ndipo analowa m'nyumba ya Mfarisi, naseama pachakudya.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsopano mmodzi mwa Afarisi anayitana Yesu kuti akadye naye ku nyumba kwake ndipo anapita nakakhala pa tebulo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mmodzi wa Afarisi anamuitana iye kuti akadye naye. Ndipo analowa m'nyumba ya Mfarisi, naseama pacakudya.