Luke 7:38 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adakagwada kumbuyo, ku mapazi a Yesu, akulira, nayamba kukhetsera misozi pa mapazi a Yesu, nkumaŵapukuta ndi tsitsi la kumutu kwake. Adampsompsonanso mapazi akewo, naŵadzoza ndi mafuta aja.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
naimirira kumbuyo, pa mapazi ake, nalira, nayamba kukhathamiza mapazi ake ndi misozi, nawapukuta ndi tsitsi la mutu wake, nampsompsonetsa mapazi ake, nawadzoza ndi mafuta onunkhira bwino.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anayimirira kumbuyo kwa Yesu pa mapazi ake akulira, nayamba kumadontheza misozi pa mapazi ake. Ndipo iye anapukuta mapaziwo ndi tsitsi lake, nawapsompsona ndi kuwathira mafuta onunkhirawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
naimirira kumbuyo, pa mapazi ace, nalira, nayamba kukhathamiza mapazi ace ndi misozi, nawapukuta ndi tsitsi la mutu wace, nampsompsonetsa mapazi ace, nawadzoza ndi mafuta onunkhira bwino.