Luke 7:39 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Mfarisi amene adaaitana Yesu uja ataona zimenezi, adayamba kuganiza kuti, “Munthuyu akadakhaladi mneneri, bwenzi atamdziŵa mai amene akumkhudzayu, kuti ndi wachiwerewere.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma Mfarisi, amene adamuitana Iye, pakuona, ananena mwa yekha, nati, Akadakhala mneneri uyu akadazindikira ali yani, ndi wotani mkaziyo womkhudza Iye, chifukwa ali wochimwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mfarisiyo anamuyitanayo ataona izi, anati mu mtima mwake, “Ngati munthuyu akanakhala mneneri, akanadziwa kuti akumukhudzayo ndi mayi otani, kuti ndi wochimwa.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma Mfarisi, amene adamuitana iye, pakuona, ananena mwa yekha, nati, Akadakhala mneneri uyu akadazindikira ali yani, ndi wotani mkaziyo womkhudza iye, cifukwa ali wocimwa.